Madalitso onse, a m’banja omwe, acokera kwa Mulungu
Nyimbo vokwerera; ya Solomo.
1 Akapanda kumanga nyumba Yehova,
Akuimanga agwiritsa nchito cabe;
Akapanda kusunga mudzi Yehoya,
Mlonda adikira cabe.
2 Kuli cabe kwa inu Rulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,
Kudya mkate wosautsa kuupeza;
Kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ace ngati m’tulo.
3 Taonani ana ndiwo colandira ca kwa Yehova;
Cipatso ca m’mimba ndico mphotho yace.
4 Ana a ubwana wace wa munthu
Akunga mibvi m’dzanja lace la ciphona.
5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lace:
Sadzacita manyazi iwo,
Pakulankhula nao adani kucipata.