Afulumizidwa anthu kulemekeza Yehova
Nyimbo vokwerera,
1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse,
Akuimirira m’nyumba ya Yehova usiku,
2 Kwezani manja anu ku malo oyera,
Nimulemekeze Yehova.
3 Yehova, ali m’Ziyoni, akudalitseni;
Ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.