Mulungu alemekezedwe pa cifundo cace
1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
2 Yamikani Mulungu wa milungu:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
3 Yamikani Mbuye wa ambuye:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
4 Amene yekha acita zodabwiza zazikuru:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
5 Amene analenga zakumwamba mwanzeru:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
7 Amene analenga miuni yaikuru:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
8 Dzuwa liweruze usana:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
9 Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
10 Iye amene anapandira Aaigupto ana ao oyamba:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
11 Naturutsa Israyeli pakati pao;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
13 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
14 Napititsa Israyeli pakati pace;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
15 Nakhutula Farao ndi khamu lace m’Nyanja Yofiira:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
16 Amene anatsogolera anthu ace m’cipululu:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
17 Amene anapanda mafumu akulu:
Pakuti cifundo cace ncosatha,
18 Ndipo anawapha mafumu omveka:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
19 Sihoni mfumu ya Aamori;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
20 Ndi ogi mfumu ya Basana:
Pakuti cifundo cace ncosatha.
21 Ndipo anaperekadzikolaolikhale cosiyira;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
22 Cosiyira ca kwa Israyeli mtumiki wace;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
23 Amene anatikumbukila popepuka ife;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
24 Natikwatula kwa otisautsa;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
25 Ndiye wakupatsa nyama zonse cakudya;
Pakuti cifundo cace ncosatha.
26 Yamikani Mulungu wa kumwamba,
Pakuti cifundo cace ncosatha.