Davide ayamika Mulungu pa kukhulupirika kwace, naneneratu kuti mafumu onse adzatero
Salmo la Davide.
1 Ndidzakuyamikani ndi mtima wangawonse;
Ndidzayimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu,
2 Ndidzagwadira kuloza ku Kacisi wanu woyera,
Ndi kuyamika dzina lanu,
Cifukwa ca cifundo canu ndi coonadi canu;
Popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
3 Tsiku loitana ine, munandiyankha,
Munandilimbitsa ndi mphamvu m’moyo mwanga.
4 Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,
Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.
5 Ndipo adzayimbira njira za Yehova;
Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukuru.
6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;
Koma wodzikuza amdziwira kutali.
7 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;
Mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,
Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
8 Yehova adzanditsirizira za kwa ine:
Cifundo canu, Yehova, cifikira ku nthawi zonse:
Musasiye nchito za manja anu.