Davide apempha Mulungu amlanditse kwa mdani woipa wamphamvu
Kwa Mkulu wa nsembe; Salmo la Davide.
1 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;
Ndisungeni kwa munthu waciwawa;
2 Amene adzipanga zoipa mumtima mwao;
Masiku onse amemeza nkhondo.
3 Anola lilime lao ngati njoka;
Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.
4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m’manja mwa woipa;
Ndisungeni kwa munthu waciwawa;
Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
5 Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe;
Anacha ukonde m’mphepete mwa njira;
Anandichera makwekwe.
6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;
Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga,
Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;
Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.
9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,
Coipa ca milomo yao ciwaphimbe.
10 Makala amoto awagwere;
Aponyedwe kumoto;
M’maenje ozama, kuti asaukenso.
11 Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi;
Coipa cidzamsaka munthu waciwawa kuti cimgwetse.
12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,
Ndi kuweruzira aumphawi,
13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;
Oongoka mtima adzakhala pamaso panu,