Davide apempha Mulungu amthandize poyesedwa ndi zoipa
Salmo la Davide.
1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;
Mundicherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.
2 Pempherolanga liikike ngaticofukiza pamaso panu;
Kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
3 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;
Sungani pakhomo pa milomo yanga.
4 Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa,
Kucita nchito zoipa
Ndi anthu akucita zopanda pace;
Ndipo ndisadye zankhuli zao.
5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo:
Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;
Mutu wanga usakane:
Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;
Nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.
7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,
Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.
8 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;
Ndithawira kwa Inu; musataye moyowanga.
9 Mundisunge ndisagwe mumsampha anandicherawo,
Ndisakodwe m’makwekwe a iwo ocita zopanda pace,
10 Oipa agwe pamodzi m’maukonde ao,
Kufikira nditapitirira ine.