Pemphero pakuopsedwa kwakukuru
Cilangizo ca Davide, muja anakhala m’phanga; Pemphero,
1 Ndipfuula nalo liu langa kwa Yehova;
Ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.
2 Nditsanulirakudandaulakwanga pamaso pace;
Ndionetsa msauko wanga pamaso pace.
3 Pamene mzimu wanga unakomoka m’kati mwanga, munadziwa njira yanga.
M’njira ndiyendamo anandichera msampha,
4 Penyani ku dzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;
Pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
5 Ndinapfuulira kwa inu, Yehova;
Ndina, Inu ndinu pothawirapo panga,
Gawo langa m’dziko la amoyo.
6 Tamverani kupfuula kwanga; papeza ndisauka kwambiri;
Ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.
7 Turutsani moyo wanga m’ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;
Olungama adzandizinga;
Pakuti mudzandicitira zokoma.