Davide apempha Mulungu amlanditse msanga kwa adani ace
Salmo la Davide.
1 Imvani pemphero langa, Yehova; ndicherere khutu kupemba kwanga;
Ndiyankheni mwa cikhulupiriko canu, mwa cilungamo canu.
2 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;
Pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.
3 Pakuti mdani alondola moyo wanga;
Apondereza pansr moyo wanga;
Andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;
Mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga,
5 Ndikumbukila masiku a kale lomwe;
Zija mudazicita ndilingirirapo;
Ndikamba pa ndekha za nchito ya manja anu.
6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:
Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.
7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.
Musandibisire nkhope yanu;
Ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
8 Mundimvetse cifundo canu mamawa;
Popeza ndikhulupirira Inu:
Mundidziwitse njira ndiyendemo;
Popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;
Ndibisala mwa Inu.
10 Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;
Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kucidikha.
11 Mundipatse moyo, Yehova, cifukwa ca dzina lanu;
Mwa cilungamo canu muturutse moyo wanga m’nsautso.
12 Ndipo mwa cifundo canu mundidulire adani anga,
Ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;
Pakuti ine ndine mtumiki wanu.