Cifoko ca munthu, cikhulupiriko ca Mulungu
1 Haleluya;
Ulemekeze Yehova, moyo wanga,
2 Ndidzalemekeza Yehovam’moyo mwanga;
Ndidzayimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
3 Musamakhulupirira zinduna,
Kapena mwana wa munthu, amene mulibe cipulumutso mwa iye.
4 Mpweya wace ucoka, abwerera kumka ku nthaka yace;
Tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zace zitayika.
5 Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize,
Ciyembekezo cace ciri pa Yehova, Mulungu wace;
6 Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi,
Nyanja ndi zonse ziri m’mwemo;
Ndiye wakusunga coonadi kosatha:
7 Ndiye wakucitira ciweruzo osautsika;
Ndiye wakupatsa anjala cakudya;
Yehova amasula akaidi;
8 Yehova apenyetsa osaona;
Yehova aongoletsa onse owerama;
Yehova akonda olungama;
9 Yehova asunga alendo;
Agwiriziza mwana wamasiye mkazi wamasiye;
Koma akhotetsa njira ya oipa.
10 Yehova adzacita ufumu kosatha,
Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwo mibadwo.
Haleluya.