Masalmo 147

Alemekeze dzina la Mulungu cifukwa ca zokoma amacitira anthu ace

1 Haleluya;

Pakuti kuyimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;

Pakuti cikondwetsa ici, cilemekezo ciyenera.

2 Yehova amanga Yerusalemu;

Asokolotsa otayika a Israyeli.

3 Aciritsa osweka mtima,

Namanga mabala ao.

4 Awerenga nyenyezi momwe ziri;

Azicha maina zonsezi.

5 Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri;

Nzeru yace njosatha.

6 Yehova agwiriziza ofatsa;

Atsitsira oipa pansi.

7 Yamikani Yehova ndi kuthira mang’ombe;

Myimbireni Mulungu wathu zamlemekeza pazeze:

8 Amene aphimba thambo ndi mitambo,

Amene akonzera mvula nthaka,

Amene aphukitsa msipu pamapiri.

9 Amene apatsa zoweta cakudya cao,

Ana a khungubwi alikulira.

10 Mphamvu ya kavalo siimkonda:

Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye,

Iwo akuyembekeza cifundo cace.

12 Yerusalemu, lemekezani Yehova;

Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.

13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:

Anadalitsa ana anu m’kati mwanu.

14 Ndiyeamene akhalitsamalireanu mumtendere;

Akukhutitsani ndi tirigu wakuca bwino.

15 Atumiza lamulo lace ku dziko lapansi;

Mau ace athamanga liwiro.

16 Apatsa cipale cofewa ngati ubweya;

Awaza cisanu ngati phulusa.

17 Aponya matalala ace ngati zidutsu:

Adzaima ndani pa kuzizira kwace?

18 Atumiza mau ace nazisungunula;

Aombetsa mphepo yace, ayenda madzi ace.

19 Aonetsa mau ace kwa Yakobo;

Malemba ace, ndi maweruzo ace kwa Israyeli.

20 Sanatero nao anthu amtundu wina;

Ndipo za maweruzo ace, sanawadziwa.

Haleluya.