Zolengedwa zonse zilemekeze Mulungu
1 Haleluya.
Lemekezani Yehova kocokera kumwamba;
Mlemekezeni m’misanje.
2 Mlemekezeni, angelo ace onse;
Mlemekezeni, makamu ace onse.
3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;
Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira.
4 Mlemekezeni, m’mwambamwamba,
Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5 Alemekeze dzina la Yehova;
Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;
Anazipatsa cilamulo cosatumphika.
7 Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,
Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;
8 Moto ndi matalala, cipale cofewa ndi nkhungu;
Mphepo ya namondwe, yakucita mau ace;
9 Mapiri ndi zitunda zonse;
Mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:
10 Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse;
Zokwawa, ndi mbalame zakuuluka;
11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;
Zinduna ndi oweruza onse a padziko;
12 Anyamata ndiponso anamwali;
Okalamba pamodzi ndi ana:
13 Alemekeze dzina la Yehova;
Pakuti dzina lace lokha ndi lokwezeka;
Ulemerero wace uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.
14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ace,
Cilemekezo ca okondedwa ace onse;
Ndiwo ana a Israyeli, anthu a pafupi pa Iye,
Haleluya,