Masalmo 149

Okhulupirira onse alemekeze Mulungu wao

1 Haleluya,

Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano,

Ndi cilemekezo cace mu msonkhano wa okondedwa ace.

2 Akondwere Israyeli mwa Iye amene anamlenga;

Ana a Ziyoni asekere mwa Mfumu yao.

3 Alemekeze dzina lace ndi kuthira mang’ombe;

Amyimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

4 Popeza Yehova akondwera nao anthu ace;

Adzakometsa ofatsa ndi cipulumutso,

5 Okondedwa ace atumphe mokondwera m’ulemu:

Apfuule mokondwera pamakama pao,

6 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,

Ndi lupanga lakuthwa konse konse m’dzanja lao;

7 Kubwezera cilango akunja,

Ndi kulanga mitundu ya anthu;

8 Kumanga mafumu ao ndi maunyolo,

Ndi omveka ao ndi majerejede acitsulo;

9 Kuwacitira ciweruzo colembedwaco:

Ulemu wa okondedwa ace onse ndi uwu.

Haleluya.