Zocitira miyambi
1 MIYAMBI ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli.
2 Kudziwa nzeru ndi mwambo;
Kuzindikira mau ozindikiritsa;
3 Kulandira mwambo wakusamalira macitidwe,
Cilungamo, ciweruzo ndi zolunjika;
4 Kucenjeza acibwana,
Kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;
5 Kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;
Ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;
6 Kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lace,
Mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.
Munthu asalole oipa amcete
7 Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca kudziwa;
Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.
8 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,
Ndi kusasiya cilangizo ca amako
9 Pakuti izi ndi korona wa cisomo pamtu pako,
Ndi mkanda pakhosi pako.
10 Mwananga, akakukopa ocimwa usalole.
11 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,
Tilalire osacimwa opanda cifukwa;
12 Tiwameze ali ndi moyo ngati manda,
Ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;
13 Tidzapeza cuma conse ca mtengo wace,
Tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;
14 Udzacita nafe maere,
Tonse tidzakhala ndi cibeti cimodzi;
15 Mwananga, usayende nao m’njira;
Letsa phazi lako ku mayendedwe ao;
16 Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,
Afulumira kukhetsa mwazi.
17 Pakuti kuchera msampha pamaso pa mbalame ndi cabe;
18 Ndipo awa abisalira mwazi wao wao, alalira miyoyo yao yao.
19 Mayendedwe a yense wopindula cuma monyenga ngotere;
Cilanda moyo wa eni ace,
Ceniezo la Nzeru
20 Nzeru ipfuula panja;
Imveketsa mau ace pabwalo;
21 Iitana posonkhana anthu polowera pacipata;
M’mudzi inena mau ace;
22 Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu?
Onyoza ndi kukonda kunyoza,
Opusa ndi kuda nzeru?
23 Tembenukani pamene ndikudzudzulani;
Taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,
Ndikudziwitsani mau anga.
24 Cifukwa ndaitana, ndipo munakana;
Ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;
25 Koma munapeputsa uphungu wangawonse,
Ndi kukana kudzudzula kwanga.
26 Inetu ndidzacitiraciphwete tsoka lanu,
Ndidzatonyola pakudza mantha anu;
27 Pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,
Ndi pofika tsoka lanu ngati kabvumvulu;
Pakudza kwa inu bvuto ndi nsautso.
28 Pamenepo adzandiitana, koma sindidzabvomera;
Adzandifunatu, osandipeza ai;
29 Cifukwa anada nzeru,
Sanafuna kuopa Yehova;
30 Anakana uphungu wanga,
Nanyoza kudzudzula kwanga konse;
31 Momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,
Nadzakhuta zolingalira zao.
32 Pakuti kubwerera m’mbuyo kwa acibwana kudzawapha;
Ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
33 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,
Nadzakhala phe osaopa zoipa,