Miyambi 4

Ceniezo lakuti afune Nzeru nalewe njira za oipa

1 Ananu, mverani mwambo wa atate,

Nimuchere makutu mukadziwe luntha;

2 Pakuti ndikuphunzitsani zabwino;

Musasiye cilangizo canga.

3 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,

Wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabala wina.

4 Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,

Mtima wako uumirire mau anga;

Sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

5 Tenga nzeru, tenga luntha;

Usaiwale, usapatuke pa mau a m’kamwa mwanga;

6 Usasiye nzeru, ndipo Idzakusunga;

Uikonde, idzakucinjiriza.

7 Nzeru ipambana, tatenga nzeru;

M’kutenga kwako konseko utenge luntha.

8 Uilemekeze, ndipo idzakukweza;

Idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

9 Idzaika cisada ca cisomo pamtu pako;

Idzakupatsa korona wokongola.

10 Tamvera mwananga, nulandire mau anga;

Ndipo zaka za moyo wako zidzacuruka.

11 Ndakuphunzitsa m’njira ya nzeru,

Ndakuyendetsa m’mayendedwe olungama.

12 Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;

Ukathamanga, sudzapunthwa.

13 Gwira mwambo, osauleka;

Uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.

14 Usalowe m’mayendedwe ocimwa,

Usayende m’njira ya oipa.

15 Pewapo, osapitamo;

Patukapo, nupitirire.

16 Pakuti akapanda kucita zoipa, samagona;

Ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwacokera.

17 Pakuti amadya cakudya ca ucimo,

Namwa vinyo wa cifwamba.

18 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca,

Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.

19 Njira ya oipa ikunga mdima;

Sadziwa cimene ciwapunthwitsa,

20 Mwananga, tamvera mau anga;

Cherera makutu ku zonena zanga.

21 Asacoke ku maso ako;

Uwasunge m’kati mwa mtima wako.

22 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,

Nalamitsa thupi lao lonse.

23 Cinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;

Pakuti magwero a moyo aturukamo.

24 Tasiya m’kamwa mokhota,

Uike patari milomo yopotoka.

25 Maso ako ayang’ane m’tsogolo,

Zikope zako zipenye moongoka,

26 Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;

Njira zako zonse zikonzeke.

27 Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere;

Suntha phazi lako kusiya zoipa.