1 Ha, mapazi ako akongola m’zikwakwata,
Mwana wamkaziwe wa mfumu!
Pozinga m’cuuno mwako pakunga zonyezimira,
Nchito ya manja a mmisiri waluso.
2 Pamcombo pako pakunga cikho coulungika,
Cosasowamo vinyo wosanganika:
Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu
Wozingidwa ndi akakombo.
3 Maere ako akunga ana awiri a nswala
Anabadwa limodzi.
4 Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;
Maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,
A pa cipata ca Batirabimu;
Mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebano
Imene iloza ku Damasiko.
5 Mutu wako ukunga Karimeli,
Ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsaru yakuda;
Mfumu yamangidwa ndi nkhata zace ngati wamsinga.
6 Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,
Bwenziwe, m’zokondweretsa!
7 Msinkhu wakowu ukunga mlaza,
Maere ako akunga matsango amphesa,
8 Ndinati, Ndikakwera pamlazapo,
Ndikagwira nthambi zace:
Maere ako ange ngati matsango amphesa,
Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;
9 M’kamwa mwako munge ngati vinyo woposa,
Womeza tseketeke bwenzi langa,
Wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
10 Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo,
Ndine amene andifunayo.
11 Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda;
Titsotse m’miraga.
12 Tilawire kunka ku minda yamipesa;
Tiyang’ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso,
Makangaza ndi kutuwa maluwa ace;
Pompo ndidzakupatsa cikondi canga,
13 Mandimu anunkhira,
Ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundu mitundu, zakale ndi zatsopano,
Zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.