Yona 3

Yona ku Nineve, Kulapa kwa a ku Nineve

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yaciwiri, ndi kuti,

2 Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukuru uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.

3 Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Nineve, monga mwa mau a Yehova. Koma Nineve ndiwo mudzi waukuru pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.

4 Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Nineve adzapasuka.

5 Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng’ono wa iwowa.

6 Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m’mapulusa.

7 Ndipo analalikira, nanena m’Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng’ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;

8 koma zipfundidwe ndi ciguduli munthu ndi nyama, nizipfuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yace yoipa, ndi ciwawa ciri m’manja mwace.

9 Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wace waukali, kuti tisatayike,

10 Ndipo Mulungu anaona nchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka coipa adanenaci kuti adzawacitira, osacicita.