Pemphero la Yona ali m’mimba mwa cinsomba
1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m’mimba mwa nsombayo.
2 Ndipo anati,
Ndinaitana Yehova m’nsautso yanga,
Ndipo anandiyankha ine;
Ndinapfuula ndiri m’mimba ya manda,
Ndipo munamva mau anga.
3 Pakuti munandiponya mwakuya m’kati mwa nyanja,
Ndipo madzi anandizinga;
Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu;
Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.
5 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,
Madzi akuya anandizungulira,
Kayandeyande wa m’nyanja anandikulunga mutu.
6 Ndinatsikira ku matsinde a mapiri,
Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;
Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7 Pokomoka moyo wanga m’kati mwanga ndinakumbukila Yehova;
Ndi pemphero langa linafikira Inu m’Kacisi wanu wopatulika.
8 Iwo osamalira mabodza opanda pace
Ataya cifundo cao cao.
9 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,
Ndidzakwaniritsacowindacanga.
Cipulumutso nca Yehova.
10 Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.