Bilidadi akuti munthu sayenera kudziyesa wolungama pamaso pa Mulungu
1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2 Kulamulira ndi kuopsa kuti ndi Iye;
Acita mtendere pa zam’mwamba zace.
3 Ngati awerengedwa makamu ace?
Ndipo ndaniyo, kuunika kwace sikumturukira?
4 Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?
Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
5 Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;
Ndi nyenyezi siziyera pamaso pace;
6 Kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!
Ndi wobadwa ndi munthu, ndiyo nyongolotsi!