1 Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?
Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ace?
2 Alipo akusendeza malire;
Alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.
3 Akankhizira kwao buru wa amasiye,
Atenga ng’ombe ya mfedwa ikhale cikole.
4 Apambukitsa aumphawi m’njira;
Osauka a padziko abisala pamodzi.
5 Taonani, ngati mbidzi za m’cipululu
Aturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya;
Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao.
6 Atema dzinthu zao m’munda;
Natola khunkha m’munda wampesa wa woipa.
7 Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala,
Alibe copfunda pacisanu.
8 Abvumbwa ndi mvula kumapiri,
Nafukata thanthwe posowa pousapo.
9 Akwatula wamasiye kubere,
Natenga cikole cobvala ca osauka;
10 Momwemo ayenda amarisece opanda cobvala,
Nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.
11 M’kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;
Aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.
12 M’mudzi waukuru anthu abuula alinkufa;
Ndi moyo wa iwo olasidwa upfuula;
Koma Mulungu sasamalira coipaco.
13 Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,
Sadziwa njira zace,
Sasunga mayendedwe ace.
14 Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;
Ndi usiku asanduka mbala.
15 Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira,
Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;
Nabvala cophimba pankhope pace.
16 Kuli mdima aboola nyumba,
Usana adzitsekera,
Osadziwa kuunika.
17 Pakuti iwo onse auyesa m’mawa mthunzi wa imfa;
Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18 Atengedwa ngati coyandama pamadzi;
Gawo lao litembereredwa padziko;
Sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.
19 Cirala ndi dzuwa zitha madzi a cipale cofewa,
Momwemo manda acita nao ocimwa.
20 M’mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera.
Sadzamkumbukilanso;
Ndipo cosalungama cidzatyoledwa ngati mtengo.
21 Alusira cumba wosabala,
Osamcitira wamasiye cokoma.
22 Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yace;
Iwo aukanso m’mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.
23 Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;
Koma maso ace ali pa njira zao.
24 Akwezeka; m’kamphindi kuti zi;
Inde atsitsidwa, acotsedwa monga onse ena,
Adutidwa ngati tirigu ngala zace.
25 Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndiri wabodza,
Ndi kuyesa mau anga opanda pace?