1 Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,
Kumanda kwandikonzekeratu.
2 Zoonadi, ali nane ondiseka;
Ndi diso langa liri cipenyere m’kundiwindula kwao.
3 Mupatse cigwiriro tsono, mundikhalire cikole Inu nokha kwanu;
Ndani adzapangana nane kundilipirira?
4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;
Cifukwa cace simudzawakuza.
5 Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo,
M’maso mwa ana ace mudzada.
6 Anandiyesanso nthanthi za anthu;
Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace.
7 M’diso mwanga mucita cizirezire cifukwa ca cisoni,
Ndi ziwalo zanga zonse ziribe cithunzi.
8 Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,
Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.
9 Koma wolungama asungitsa njira yace,
Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10 Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;
Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11 Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,
Zace zace zomwe za mtima wanga.
12 Zisanduliza usiku ukhale usana;
Kuunika kuyandikana ndi mdima.
13 Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;
Ndikayala pogona panga mumdima.
14 Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;
Kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;
15 Ciri kuti ciyembekezo canga?
Inde, ciyembekezo canga adzaciona ndani?
16 Cidzatsikira ku mipingiridzo ya kumanda,
Pamene tipumulira pamodzi kupfumbi.