Yesaya 4

Tsiku la Mulungu, kuyeretsedwa kwa Yerusalemu

1 Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya cakudya cathu cathu ndi kubvala zobvala zathu zathu; koma tichedwe dzina lako; cotsa citonzo cathu.

2 Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, cipatso ca nthaka cidzakhala cokometsetsa ndi cokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israyeli.

3 Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m’Ziyoni, ndi iye amene atsala m’Yerusalemu, adzachedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m’Yerusalemu;

4 pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kucokera pakatipo, ndi mzimu wa ciweruziro, ndi mzimu wakutentha.

5 Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ace, mtambo ndi utsi usana, ndi kung’azimira kwa malawi a moto usiku; cifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa cophimba.

6 Ndipo padzakhala cihema ca mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.