Yesaya 15

Aneneratu za kuonongeka kwa Moabu

1 Katundu wa Moabu.

Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe.

2 Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa.

3 M’makwalala mwao adzimangira ciguduli m’cuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m’malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.

4 Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m’kati mwace.

5 Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m’njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko.

6 Pakuti pa madzi a Nimirimi padzakhala mabwinja; papeza udzu wafota, msipu watha.

7 Cifukwa cace zocuruka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo ku mtsinje wa mabango.

8 Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Moabu; kukuwa kwace kwafikira ku Eglaimu, ndi kukuwa kwace kwafikira ku Beerelimu.

9 Pakuti madzi a Dimoni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa! Dimoni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Moabu, ndi pa otsala am’dziko.