Yeremiya 47

Aneneratu za citsutso ca Afilisti

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.

2 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kuturuka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse ziri m’mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m’dziko adzakuwa.

3 Pomveka migugu ya ziboda za olimba ane, pogumukira magareta ace, ndi pophokosera njinga zace, atate sadzaceukira ana ao cifukwa ca kulefuka kwa manja ao;

4 cifukwa ca tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Turo ndi Zidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a cisumbu ca Kafitori.

5 Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m’cidikha cao; udzadziceka masiku angati?

6 Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala cete iwe? dzilonge wekha m’banzi lako; puma, nukhale cete.

7 Udzakhala cete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? za Asikeloni, ndi za m’mbali mwa nyanja, pamenepo analiika.