1 Mwenzi utakhala ngati mlongwanga,
Woyamwa pa bere la amai!
Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;
Osandinyoza munthu.
2 Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m’nyumba ya amai,
Kuti andilange mwambo; Ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,
Ndi madzi a makangaza anga.
3 Dzanja lamanzere lace akadanditsamiritsa kumutu,
Lamanja lace ndi kundifungatira.
4 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
Muutsiranji, mugalamutsiranji cikondi,
Cisanafune mwini.
5 Ndaniyu acokera kucipululu,
Alikutsamira bwenzi lace?
Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:
Pomwepo amako anali mkusauka nawe,
Pomwepo wakukubala anali m’pakati pa iwe.
6 Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako;
Pakuti cikondi cilimba ngati imfa;
Njiru imangouma ngati manda:
Kung’anima kwace ndi kung’anima kwa moto,
Ngati mphezi ya Yehova,
7 Madzi ambiri sangazimitse cikondi,
Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola:
Mwamuna akapereka katundu yense wa m’nyumba yace ngati sintho la cikondi,
Akanyozedwa ndithu.
8 Tiri ndi mlongwathu wamng’ono,
Alibe maere;
Ticitirenji mlongwathu
Tsiku lokhoma unkhoswe wace?
9 Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:
Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.
10 Ndine khoma, maere anga akunga nsanja zace:
Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
11 Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni;
Nabwereka alimi mundawo;
Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.
12 Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu;
Naco cikwico, Solomo iwe,
Koma olima zipatso zace azilandira mazana awiri.
13 Namwaliwe wokhala m’minda,
Anzake amvera mau ako:
Nanenso undimvetse.
14 Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,
Dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala
Pa mapiri a mphoka,