Mkwatibwi apeza mkwati
1 Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:
Ndinamfunafuna, koma osampeza.
2 Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m’mudzi,
M’makwalala ndi m’mabwalo ace,
Ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:
Ndimfunafuna, koma osampeza.
3 Alonda akuyendayenda m’mudzi anandipeza:
Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4 Nditawapitirira pang’ono,
Ndinampeza amene moyo wanca umkonda:
Ndinamgwiriziza, osamfumbatula,
Mpaka nditamlowetsa m’nyumba ya amai,
Ngakhale m’cipinda ca wondibala.
5 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,
Pali mphoyo, ndi nswala ya kuthengo,
Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,
Mpaka cikafuna mwini.
Ulendo wa ukwati
6 Ndaniyu akwera kuturuka m’cipululu ngati utsi wa tolo,
Wonunkhira ndi nipa ndi mtanthanyerere,
Ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7 Taonani, ndi macila a Solomo;
Pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,
A mwa ngwazi za Israyeli.
8 Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:
Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace,
Cifukwa ca upandu wa usiku.
9 Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsonga
Ndi matabwa a ku Lebano.
10 Anapanga timilongoti tace ndi siliva,
Ca pansi pace ndi golidi, mpando wace ndi nsaru yakuda,
Pakati pace panayalidwa za cikondi ca ana akazi a ku Yerusalemu.
11 Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu,
Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace,
Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.