Nyimbo 2

1 Ndine duwa lofiira la ku Saroni,

Ngakhale kakombo wa kuzigwa.

2 Ngati kakombo pakati pa minga

Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.

3 Ngati maula pakati pa mitengo ya m’nkhalango,

Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna.

Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wace,

Zipatso zace zinatsekemera m’kamwa mwanga.

4 Anandifikitsa ku nyumba ya vinyo,

Mbendera yace yondizolimira inali cikondi.

5 Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula,

Pakuti ndadwala ndi cikondi.

6 Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu,

Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.

7 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,

Pali mphoyo, ndi nswala za kuthengo,

Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,

Mpaka cikafuna mwini.

8 Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,

Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.

9 Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:

Taona, aima patseri pa khoma pathu,

Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.

10 Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,

Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.

11 Pakuti, taona, cisanu catha,

Mvula yapita yaleka;

12 Maluwa aoneka pansi;

Nthawi yoyimba mbalame yafika,

Mau a njiwa namveka m’dziko lathu;

13 Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima,

Mipesa niphuka,

Inunkhira bwino.

Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.

14 Nkhunda yangawe, yokhala m’ming’alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka,

Ndipenye nkhope yako, ndimve manako;

Pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.

15 Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang’ono, amene akuononga minda yamipesa;

Pakuti m’minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.

16 Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wace:

Aweta zace pakati pa akakombo,

17 Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,

Bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala

Pa mapiri a mipata.