Mlaliki 6

Ngakhale Mulungu apatsa munthu zonse azikhumba koma mtima sukhuta nazo

1 Pali coipa ndaciona kunja kuno cifalikira mwa anthu,

2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,

3 Cinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zace ndi kucuruka, koma mtima wace osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;

4 pakuti ikudza mwacabe, nicoka mumdima, mdima nukwirira dzina lace.

5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;

6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?

7 Nchito zace zonse munthu angogwirira m’kamwa mwace, koma mtima wace sukhuta.

8 Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?

9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

10 Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.

11 Pokhala zinthu zambiri zingocurukitsa zacabe, kodi anthu aona phindu lanji?

12 Pakuti ndani adziwa comwe ciri cabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wace wacabe umene autsiriza ngati mthunzi? pakuti ndani adzauza munthu cimene cidzaoneka m’tsogolo mwace kunja kuno?