Malangizo a kuopa, kukhulupira, ndi kumvera Yehova
1 Mwananga, usaiwale malamulo anga,
Mtima wako usunge malangizo anga;
2 Pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,
Ndi zaka za moyo ndi mtendere.
3 Cifundo ndi coonadi zisakusiye;
Uzimange pakhosi pako;
Uzilembe pamtima pako;
4 Motero udzapezakisomo ndi nzeru yabwino,
Pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,
Osacirikizika pa luntha lako;
6 Umlemekeze m’njira zako zonse,
Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
7 Usadziyese wekha wanzeru;
Opa Yehova, nupatuke pazoipa;
8 Mitsempha yako idzalandirapo moyo,
Ndi mafupa ako uwisi.
9 Lemekeza Yehova ndi cuma cako,
Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;
10 Motero nkhokwe zako zidzangoti the,
Mbiya zako zidzasefuka vinyo.
11 Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,
Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;
12 Pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;
Monga atate mwana amene akondwera naye.
Phindu la Nzeru
13 Wodala ndi wopeza nzeru,
Ndi woona luntha;
14 Pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva,
Phindu lace liposa golidi woyengeka.
15 Mtengo wace uposa ngale;
Ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.
16 Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lace;
Cuma ndi ulemu m’dzanja lace lamanzere.
17 Njira zace ziri zokondweretsa,
Mayendedwe ace onse ndiwo mtendere.
18 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;
Wakulumirira ngwodala.
19 Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;
Naika zamwamba ndi luntha.
20 Zakuya zinang’ambika ndi kudziwakwace;
Thambo ligwetsa mame.
21 Mwananga, zisacokere ku maso ako;
Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;
22 Ndipo mtima wako udzatengapo moyo,
Ndi khosi lako cisomo.
23 Pompo udzayenda m’njira yako osaopa,
Osapunthwa phazi lako.
24 Ukagona, sudzacita mantha;
Udzagona tulo tokondweretsa.
25 Usaope zoopsya zodzidzimutsa,
Ngakhale zikadza zopasula oipa;
26 Pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,
Nadzasunga phazi lako lingakodwe.
Malangizo ena osiyana
27 Oyenera kulandira zabwino usawamane;
Pokhoza dzanja lako kuwacitira zabwino.
28 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,
Ndipo mawa ndidzakupatsa;
Pokhala uli nako kanthu.
29 Usapangire mnzako ciwembu;
Popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.
30 Usakangane ndi munthu cabe,
Ngati sanakucitira coipa,
31 Usacitire nsanje munthu waciwawa;
Usasankhe njira yace iri yonse.
32 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;
Koma cinsinsi cace ciri ndi oongoka.
33 Mulungu atemberera za m’nyumba ya woipa;
Koma adalitsa mokhalamo olungama.
34 Anyozadi akunyoza,
Koma apatsa akufatsa cisomo.
35 Anzeru adzalandira ulemu colowa cao;
Koma opusa adzakweza manyazi.