1 Usacitire nsanje anthu oipa, Ngakhale kufuna kukhala nao;
2 Pakuti mtima wao ulingalira za cionongeko;
Milomo yao ilankhula za mphulupulu.
3 Nzeru imangitsa nyumba;
Luntha liikhazikitsa.
4 Kudziwa kudzaza zipinda zace
Ndi cuma conse cofunika ca mtengo wace.
5 Mwamuna wanzeru ngwamphamvu;
Munthu wodziwa ankabe nalimba.
6 Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo,
Ndi kupulumuka pocuruka aphungu,
7 Nzeru itarikira citsiru;
Satsegula pakamwa kubwalo.
8 Wolingalira zakucita zoipa
Anthu adzamcha waciwembu.
9 Maganizo opusa ndiwo cimo;
Wonyoza anyansa anthu.
10 Ukalefuka tsiku la tsoka
Mphamvu yako icepa.
11 Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse;
Omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.
12 Ukanena, Taonani, sitinadziwa cimeneci;
Kodi woyesa mitima sacizindikira ici?
Ndi wosunga moyo wako kodi sacidziwa?
Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa macitidwe ace?
13 Mwananga, idya uci pakuti ngwabwino,
Ndi cisa cace citsekemera m’kamwamwako;
14 Potero udzadziwa kuti nzeru iri yotero m’moyo wako;
Ngati waipeza padzakhala mphotho,
Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.
15 Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama;
Usapasule popuma iyepo.
16 Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso;
Koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.
17 Usakondwere pakugwa mdani wako;
Mtima wako usasekere pokhumudwa iye;
18 Kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa,
Ndi kuleka kumkwiyira.
19 Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa;
Ngakhale kucitira nsanje amphulupulu;
20 Pakuti woipayo sadzalandira mphotho;
Nyali ya amphulupulu idzazima.
21 Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe,
Osadudukira anthu osinthasintha.
22 Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka;
Ndipo ndani adziwa cionongeko ca zaka zao?
23 Izinso ziri za anzeru.
Poweruza cetera siliri labwino.
24 Wonenakwa woipa, Wolungama iwe;
Magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira,
25 Omwe amdzudzula adzasekera,
Nadzadalitsika ndithu.
26 Wobwezera mau oongoka
Apsompsona milomo.
27 Longosola nchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda;
Pambuyo pace ndi kumanga nyumba yako.
28 Usacitire mnzako umboni womtsutsa opanda cifukwa;
Kodi udzanyenga ndi milomo yako?
29 Usanene, Ndidzamcitira zomwezo anandicitira ine;
Ndidzabwereza munthuyo monga mwa macitidwe ace.
30 Ndinapita pa munda wa wolesi,
Polima mphesa munthu wosowa nzeru.
31 Taonani, ponsepo panamera minga,
Ndi kuwirirapo khwisa;
Chinga lace lamiyala ndi kupasuka.
32 Pamenepo ndinayang’ana ndi kuganizira,
Ndinaona ndi kulandira mwambo.
33 Tulo tapang’ono, kungoodzera pang’ono,
Kungomanga manja pang’ono m’kugona,
34 Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala;
Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.