Ukoma ndi phindu tace la Nzeru
1 Mwananga, ukalandira mau anga,
Ndi kusunga malamulo anga;
2 Kucherera makutu ako kunzeru,
Kulozetsa mtima wako kukuzindikira;
3 Ukaitananso luntha,
Ndi kupfuulira kuti ukazindikire;
4 Ukaifunafuna ngati siliva,
Ndi kuipwaira ngati cuma cobisika;
5 Pompo udzazindikira kuopa Yehova
Ndi kumdziwadi Mulungu.
6 Pakuti Yehova apatsa nzeru;
Kudziwa ndi kuzindikira kuturuka m’kamwa mwace;
7 Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;
Ndiye cikopa ca oyenda molunjika;
8 Kuti acinjirize njira za ciweruzo,
Nadikire khwalala la opatulidwa ace.
9 Pamenepo udzazindikira cilungamo ndi ciweruzo,
Zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa m’mtima mwako,
Moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,
11 Kulingalira kudzakudikira,
Kuzindikira kudzakucinjiriza;
12 Kukupulumutsa ku njira yoipa,
Kwa anthu onena zokhota;
13 Akusiya mayendedwe olungama,
Akayende m’njira za mdima;
14 Omwe asangalala pocita zoipa,
Nakondwera ndi zokhota zoipa;
15 Amene apotoza njira zao,
Nakhotetsa mayendedwe ao;
16 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi waciwerewere,
Kwa mkazi wacilendo wosyasyalika ndi mau ace;
17 Wosiya bwenzi la ubwana wace,
Naiwala cipangano ca Mulungu wace;
18 Nyumba yace itsikira kuimfa,
Ndi mayendedwe ace kwa akufa;
19 Onse akunka kwa iye sabweranso,
Safika ku njira za moyo;
20 Nzeru idzakuyendetsa m’njira ya anthu abwino,
Kuti usunge mayendedwe a olungama.
21 Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko,
Angwiro nadzatsalamo.
22 Koma oipa adzalikhidwa m’dziko,
Aciwembu adzazulidwamo.