1 Wopanduka afunafuna niro cace,
Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2 Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;
Koma kungobvumbulutsa za m’mtima mwace.
3 Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;
Manyazi natsagana ndi citonzo.
4 Mau a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;
Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankhu sikuli kwabwino,
Ngakhale kucitira cetera wolungama.
6 Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;
Ndipo m’kamwa mwace muputa kukwapulidwa.
7 M’kamwa mwa wopusa mumuononga,
Milomo yace ikhala msampha wa moyo wace.
8 Mau a kazitape akunga zakudya zolongosoka,
Zotsikira m’kati mwa mimba.
9 Wogwira nchito mwaulesi
Ndiye mbale wace wa wosakaza.
10 Dzina la Yehova ndilo linga lolimba;
Wolungama athamangiramo napulumuka.
11 Cuma ca wolemera ndico mudzi wace wolimba;
Alingalira kuti ndico khoma lalitari.
12 Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;
Koma cifatso citsogolera ulemu.
13 Wobwezera mau asanamvetse apusa,
Nadzicititsa manyazi.
14 Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;
Koma ndani angatukule mtima wosweka?
15 Mtima wa wozindikira umaphunzira;
Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16 Mtulo wa munthu umtsegulira njira,
Numfikitsa pamaso pa akuru.
17 Woyamba kudzinenera ayang’anika wolungama;
Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.
18 Ula uletsa makangano,
Nulekanitsa amphamvu.
19 Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta,
Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta;
Makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20 Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m’kamwa mwace;
Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.
21 Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;
Wolikonda adzadya zipatso zace.
22 Wopeza mkazi apeza cinthu cabwino;
Yehova amkomera mtima.
23 Wosauka amadandaulira;
Koma wolemera ayankha mwaukali.
24 Woyanjana ndi ambiri angodziononga;
Koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.