Miyambi 15

1 Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;

Koma mau owawitsa aputa msunamo.

2 Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;

Koma m’kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.

3 Maso a Yehova ali ponseponse,

Nayang’anira oipa ndi abwino.

4 Kuciza lilime ndiko mtengo wa moyo;

Koma likakhota liswa moyo.

5 Citsiru cipeputsa mwambo wa atate wace;

Koma wosamalira cidzudzulo amacenjera.

6 M’nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;

Koma m’phindu la woipa muli bvuto,

7 Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,

Koma mtima wa opusa suli wolungama.

8 Nsembe ya oipa inyansa Yehova;

Koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.

9 Njira ya oipa inyansa Yehova;

Koma akonda wolondola cilungamo.

10 Wosiya njira adzalangidwa mowawa;

Wakuda cidzudzulo adzafa.

11 Kumanda ndi kucionongeko kuli pamaso pa Yehova;

Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?

12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,

Samapita kwa anzeru.

13 Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;

Koma moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.

14 Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;

Koma m’kamwa mwa opusa mudya utsiru.

15 Masiku onse a wosauka ali oipa;

Koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

16 Zapang’ono, ulikuopa Yehova,

Zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso,

17 Kudya masamba, pali cikondano,

Kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.

18 Munthu wozaza aputa makani;

Koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

19 Mayendedwe a wolesi akunga Hnga laminga,

Koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.

20 Mwana wanzeru akondweretsa atate wace;

Koma munthu wopusa apeputsa amace.

21 Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;

Koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ace.

22 Zolingalira zizimidwa popanda upo

Koma pocuruka aphungu zikhazikika.

23 Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwace;

Ndi mau a pa nthawi yace kodi sali abwino?

24 Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,

Kuti apambuke kusiya kunsi kwa manda.

25 Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;

Koma adzalembera mkazi wamasiye malire ace,

26 Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;

Koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.

27 Wopindula monyenga abvuta nyumba yace;

Koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

28 Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;

Koma m’kamwa mwa ocimwa mutsanulira zoipa.

29 Yehova atarikira oipa;

Koma pemphero la olungama alimvera.

30 Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;

Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31 Khutu lomvera cidzudzulo ca moyo

Lidzakhalabe mwa anzeru.

32 Wokana mwambo apeputsa moyo wace;

Koma wosamalira cidzudzulo amatenga nzeru.

33 Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;

Ndipo cifatso citsogolera ulemu.