1 Mkazi yense wanzeru amanga banja lace;
Koma wopusa alipasula ndi manja ace.
2 Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;
Koma wokhota m’njira yace amnyoza,
3 M’kamwa mwa citsiru muli ntyole ya kudzikuza;
Koma milomo ya anzeru Idzawasunga.
4 Popanda zoweta modyera muti see;
Koma mphamvu ya ng’ombe icurukitsa phindu.
5 Mboni yokhulupirika sidzanama;
Koma mboni yonyenga imalankhula zonama.
6 Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;
Koma wozindikira saona bvuto m’kuphunzira.
7 Pita pamaso pa munthu wopusa,
Sudzazindikira milomo yakudziwa.
8 Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace;
Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo.
9 Zitsiru zinyoza kuparamula;
Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano.
10 Mtima udziwa kuwawa kwace kwace;
Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.
11 Nyumba ya oipa idzapasuka;
Koma hema wa oongoka mtima adzakula.
12 Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;
Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
13 Ngakhale m’kuseka mtima uwawa;
Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni.
14 Wobwerera m’mbuyo m’mtima adzakhuta njira zace;
Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
15 Wacibwana akhulupirira mau onse;
Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace.
16 Wanzeru amaopa nasiya zoipa;
Koma wopusa amanyada osatekeseka.
17 Wokangaza kukwiya adzacita utsiru;
Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.
18 Acibwana amalandira colowa ca utsiru;
Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.
19 Oipa amagwadira abwino,
Ndi ocimwa pa makomo a olungama.
20 Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;
Koma akukonda wolemera acuruka.
21 Wonyoza anzace acimwa;
Koma wocitira osauka cifundo adala.
22 Kodi oganizira zoipa sasocera?
Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.
23 M’nchito zonse muli phindu;
Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.
24 Korona wa anzeru ndi cuma cao;
Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25 Mboni yoona imalanditsa miyoyo;
Koma wolankhula zonama angonyenga.
26 Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;
Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.
27 Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,
Kupatutsa ku misampha ya imfa.
28 Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;
Koma popanda anthu kalonga aonongeka.
29 Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;
Koma wansontho akuza utsiru.
30 Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;
Koma nsanje ibvunditsa mafupa.
31 Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace;
Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.
32 Wocimwa adzakankhidwa m’kuipa kwace;
Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira,
33 Nzeru ikhalabe m’mtima wa wozindikira,
Nidziwika pakati pa opusa.
34 Cilungamo cikuza mtundu wa anthu;
Koma cimo licititsa pfuko manyazi.
35 Mfumu ikomera mtima kapolo wocita mwanzeru;
Koma idzakwiyira wocititsa manyazi.