1 Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;
Koma wonyoza samvera cidzudzulo.
2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwace;
Koma moyo wa aciwembu udzadya ciwawa.
3 Wogwira pakamwa pace asunga moyo wace;
Koma woyasamula milomo yace adzaonongeka.
4 Moyo wa wolesi ukhumba osalandira kanthu;
Koma moyo wa akhama udzalemera.
5 Wolungama ada mau onama;
Koma woipa anyansa, nadzicititsa manyazi,
6 Cilungamo cicinjiriza woongoka m’njira;
Koma udio ugwetsa wocimwa.
7 Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;
Alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi cuma cambiri.
8 Ciombolo ca moyo wa munthu ndico cuma cace;
Koma wosauka samva cidzudzulo.
9 Kuunika kwa olungama kukondwa;
Koma nyali ya oipa idzazima.
10 Kudzikuza kupikisanitsa;
Koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.
11 Cuma colandiridwa mokangaza cidzacepa;
Koma wokundika ndi dzanja adzaona zocuruka.
12 Ciyembekezo cozengereza cidwalitsa mtima;
Koma pakufika cifuniroco ndico mtengo wa moyo.
13 Wonyoza mau adziononga yekha;
Koma woopa malangizo adzalandira mphotho.
14 Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,
Apatutsa ku misampha ya imfa.
15 Nzeru yabwino ipatsa cisomo;
Koma njira ya aciwembu iri makolokoto.
16 Yense wocenjera amacita mwanzeru:
Koma wopusa aonetsa utsiru.
17 Mthenga wolakwa umagwa m’zoipa;
Koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.
18 Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;
Koma wolabadira cidzudzulo adzalemekezedwa.
19 Cifuniro cikondweretsa moyo citacitidwa;
Koma kusiya zoipa kunyansa opusa,
20 Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:
Koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.
21 Zoipa zilondola ocimwa;
Koma olungama adzalandira mphotho yabwino.
22 Wabwino asiyira zidzukulu zace colowa cabwino;
Koma wocimwa angosungira wolungama cuma cace.
23 M’kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;
Koma zinazo zimaonongeka posowa ciweruzo.
24 Wolekereramwanace osammenya amuda;
Koma womkonda amyambize kumlanga.
25 Wolungama adya nakhutitsa moyo wace;
Koma mimba ya oipa idzasowa.