1 Wokonda mwambo akonda kudziwa;
Koma wakuda cidzudzulo apulukira.
2 Yehova akomera mtima munthu wabwino;
Koma munthu wa ziwembu amtsutsa,
3 Munthu sadzakhazikika ndi udio,
Muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4 Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wace;
Koma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo.
5 Maganizo a olungama ndi ciweruzo;
Koma uphungu wa oipa unyenga.
6 Mau a oipa abisalira mwazi;
Koma m’kamwa mwa olungama muwalanditsa.
7 Oipa amagwa kuli zi;
Koma banja la olungama limaimabe.
8 Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yace;
Koma wokhota mtima adzanyozedwa.
9 Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo,
Aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.
10 Wolungama asamalira moyo wa coweta cace;
Koma cifundo ca oipa ndi nkhanza.
11 Zakudyazikwanira wolima minda yace;
Koma wotsata anthu opanda pace asowa nzeru.
12 Woipa akhumba cokodwa ndi amphulupulu;
Koma muzu wa olungama umabala zipatso.
13 M’kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;
Koma wolungama amaturuka m’mabvuto.
14 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwace;
Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.
15 Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace;
Koma wanzeru amamvera uphungu.
16 Mkwiyo wa citsiru udziwika posacedwa;
Koma wanzeru amabisa manyazi.
17 Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo;
Koma mboni yonama imanyenga.
18 Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;
Koma lilime la anzeru lilamitsa.
19 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;
Koma lilime lonama likhala kamphindi.
20 Cinyengo ciri m’mitima ya oganizira zoipa;
Koma aphungu a mtendere amakondwa.
21 Palibe bvuto lidzagwera wolungama;
Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,
22 Milomo yonama inyansa Yehova;
Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23 Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;
Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24 Dzanja la akhama lidzalamulira;
Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,
25 Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;
Koma mau abwino aukondweretsa.
26 Wolungama atsogolera mnzace;
Koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27 Wolesi samaocha nyama yace anaigwira;
Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.
28 M’khwalala la cilungamo muli moyo;
M’njira ya mayendedwe ace mulibe imfa.