1 Muyeso wonyenga unyansa Yehova;
Koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.
2 Pakudza kudzikuza padzanso manyazi;
Koma nzeru iri ndi odzicepetsa,
3 Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;
Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.
4 Cuma sicithandiza tsiku la mkwiyo;
Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
5 Cilungamo ca wangwiro cimaongola njira yace;
Koma woipa adzagwa ndi zoipa zace.
6 Cilungamo ca oongoka mtima cidzawapulumutsa;
Koma aciwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
7 Pomwalira woipa cidikiro cace cionongeka;
Ciyembekezo ca ucimo cionongeka.
8 Wolungama apulumuka kubvuto;
Woipa nalowa m’malo mwace.
9 Wonyoza Mulungu aononga mnzace ndi m’kamwa mwace;
Koma olungama adzapulumuka pakudziwa,
10 Olungama akapeza bwino, mudzi usekera;
Nupfuula pakuonongeka oipa.
11 Madalitso a olungama akuza mudzi;
Koma m’kamwa mwa oipa muupasula.
12 Wopeputsa mnzace asowa nzeru;
Koma wozindikira amatonthola.
13 Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;
Koma wokhulupirika mtima abisa mau.
14 Popanda upo wanzeru anthu amagwa;
Koma pocuruka aphungu pali cipulumutso.
15 Woperekera mlendo cikole adzaphwetekwapo;
Koma wakuda cikole akhala ndi mtendere.
16 Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;
Aukali nagwiritsa cuma.
17 Wacifundo acitira moyo wace zokoma;
Koma wankhanza abvuta nyama yace.
18 Woipa alandira malipiro onyenga;
Koma wofesa cilungamo aonadi mphotho,
19 Wolimbikira cilungamo alandira moyo;
Koma wolondola zoipa adzipha yekha,
20 Okhota mtima anyansa Yehova;
Koma angwiro m’njira zao amsekeretsa.
21 Zoonadi, wocimwa sadzapulumuka cilango;
Koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.
22 Monga cipini cagolidi m’mphuno ya nkhumba,
Momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
23 Cifuniro ca olungama cifikitsa zabwino zokha;
Koma ciyembekezo ca oipa mkwiyo.
24 Alipo wogawira, nangolemerabe;
Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.
25 Mtima wa mataya udzalemera;
Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26 Womana tirigu anthu amtemberera;
Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.
27 Wopwaira ubwino afunitsa cikondwerero;
Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28 Wokhulupmra cuma cace adzagwa;
Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29 Wobvuta banja lace adzalowa m’zomsautsa;
Wopusa adzatumikira wanzeru.
30 Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo;
Ndipo wokola mtima ali wanzeru.
31 Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;
Koposa kotani woipa ndi wocimwa?