Miyambo yosiyana-siyana; Miyambo ya Sotomo
1 Mwana wanzeru akondweretsa atate;
Koma mwana wopusa amvetsa amace cisoni.
2 Cuma ca ucimo sicithangata:
Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
3 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;
Koma amainga cifuniro ca wocimwa.
4 Wocita ndi dzanja laulesi amasauka;
Koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5 Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzeru;
Koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.
6 Madalitso ali pamtu pa wolungama
Koma m’kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.
7 Amayesa wolungama wodala pamkumbukira;
Koma dzina la oipa lidzabvunda.
8 Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;
Koma citsiru colongolola cidzagwa.
9 Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;
Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.
10 Wotsinzinira acititsa cisoni;
Koma wodzudzula momveka acita mtendere.
11 M’kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;
Koma m’kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.
12 Udani upikisanitsa;
Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.
13 Nzeru ipezedwa m’milomo ya wozindikira;
Koma wopusa pamsana pace ntyole.
14 Anzeru akundika zomwe adziwa
Koma m’kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.
15 Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;
Koma umphawi wao uononga osauka.
16 Nchito za wolungama zipatsa moyo;
Koma phindu la oipa licimwitsa.
17 Wosunga mwambo ali m’njira ya moyo;
Koma wosiya cidzudzulo asocera.
18 Wobisa udani ali ndi milomo yonama;
Wonena ugogodi ndiye citsiru.
19 Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;
Koma wokhala cete acita mwanzeru.
20 Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;
Koma mtima wa oipa uli wacabe.
21 Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;
Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22 Madalitso a Yehova alemeretsa,
Saonjezerapo cisoni.
23 Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;
Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24 Comwe woipa aciopa cidzamfikira;
Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.
25 Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;
Koma olungama ndiwo maziko osatha.
26 Ngati vinyo wowawa m’mano, ndi utsi m’maso,
Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.
27 Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;
Koma zaka za oipa zidzafinimpha,
28 Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe;
Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.
29 Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;
Koma akucita zoipa adzaonongeka.
30 Wolungama sadzacotsedwa konse:
Koma oipa sadzakhalabe m’dziko.
31 M’kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;
Koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;
Koma m’kamwa mwa oipa munena zokhota,