Oweruza aweruze bwino
Salmo la Asatu.
1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,
Aweruza pakati pa milungu.
2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,
Ndi kusamalira nkhope ya oipa?
3 Weruzani osauka ndi amasiye;
Weruzani molungama ozunzika ndi osowa.
4 Pulumutsani osauka ndi aumphawi:
Alanditseni m’dzanja la oipa,
5 Sadziwa, ndipo sazindikira;
Amayendayenda mumdima;
Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,
Ndi ana a Wam’mwambamwamba nonsenu.
7 Komatu mudzafa monga anthu,
Ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.
8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;
Pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.