Davide ayimbira ulemerero wa Mulungu, ndi ulemu umene Mulungu acitira mtundu wa anthu
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Oititl. Salnto la Davide.
1 Yehova, Ambuye wathu,
Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!
Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
2 M’kamwa mwa makanda ndi oyamwamunakhazikitsamphamvu,
Cifukwa ca otsutsana ndi Inu,
Kuti muwaletse mdani ndi wobwezera cilango.
3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, nchito ya zala zanu,
Mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
4 Munthu ndani kuti mumkumbukila?
Ndi mwana wa munthu kuti muceza naye?
5 Pakuti munamcepsa pang’ono ndi Mulungu,
Munambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.
6 Munamcititsa ufumu pa nchito za manja anu;
Mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace;
7 Nkhosa ndi ng’ombe, zonsezo,
Ndi nyama za kuthengo zomwe;
8 Mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja.
Zopita m’njira za m’nyanja.
9 Yehova, Ambuye wathu,
Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!