Ulemerero ndi mphamvu ya Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Negtnolo. Salmo la Asafu. Nyimbo.
1 Mulungu adziwika mwa Yuda:
Dzina lace limveka mwa Israyeli.
2 Msasa wace unali m’Salemu, Ndipo pokhala Iye m’Ziyoni.
3 Pomwepo anatyola mibvi ya paota;
Cikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4 Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli acifwamba.
5 Olimba mtima cifunkhidwa cuma cao, agona tulo tao;
Amuna onse amphamvu asowa manja ao.
6 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,
Gareta ndi kavalo yemwe anagwa m’tulo.
7 Inu ndinu woopsa;
Ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala ciriri ndani pamaso panu?
8 Mudamveketsa ciweruzo cocokera Kumwamba;
Dziko lapansi linacita mantha, nilinakhala cete,
9 Pakuuka Mulungu kuti aweruze,
Kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.
10 Indedi, kuzaza kwace kwa munthu kudzakulemekezani;
Cotsalira ca kuzazaku mudzaciletsa.
11 Windani ndipo citirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;
Onse akumzinga abwere naco copereka ca kwa Iye amene ayenera kumuopa.
12 Iye adzadula mzimu wa akulu;
Akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.