Mulungu woweruza asiyanitsa pakati pa odzikuza ndi olungama
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Altasayeti: Salmo la Asafu. Nyimbo.
1 Tikuyamikani Inu, Mulungu; Tiyamika, pakuti dzina lanu liri pafupi;
Afotokozera zodabwiza zanu,
2 Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.
3 Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;
Ndinacirika mizati yace.
4 Ndinati kwa odzitamandira, Musamacita zodzitamandira;
Ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5 Musamakwezetsa nyanga yanu;
Musamalankhula ndi khosi louma.
6 Pakuti kukuzaku sikucokera kum’mawa,
Kapena kumadzulo, kapena kucipululu,
7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;
Acepsa wina, nakuza wina.
8 Pakuti m’dzanja la Yehova muli cikho;
Ndi vinyo wace acita thobvu;
Cidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako:
Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa
Nadzagugudiza nsenga zace.
9 Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,
Ndidzayimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;
Koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.