Masalmo 62

Posautsidwa Davide athamangira Mulungu yekha

Kwa Mlrulu wa Nyimbo, pa Jedutunu. Salmo la Davide.

1 Moyo wanga ukhalira cete Mulungu yekha:

Cipulumutso canga cifuma kwa Iye.

2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga;

Msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukuru.

3 Mudzambvumbvulukira munthu mpaka liti,

Kumupha iye, nonsenu,

Monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?

4 Komatu amkhaliraupo kuti amkankhire pansi ulemu wace;

Akondwera nao mabodza;

Adalitsa ndi m’kamwa mwao, Koma atemberera mumtima.

5 Moyo wanga, ukhalire cete Mulungu yekha;

Pakuti ciyembekezo canga cifuma kwa Iye,

6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga,

Msanje wanga, sindidzagwedezeka.

7 Pa Mulungu pali cipulumutso canga ndi ulemerero wanga:

Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.

8 Khulupirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu:

Tsanulirani mitima yanu pamaso pace:

Mulungu ndiye pothawirapo ife.

9 Indetu, anthu acabe ndi mpweya, ndipo anthu akuru ndi bodza:

Pakuwayesa apepuka;

Onse pamodzi apepuka koposa mpweya,

10 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama cifwamba;

Cikacuruka cuma musakhazikepo mitima yanu.

11 Mulungu ananena kamodzi, ndinacimva kawiri:

Kuti mphamvu ndi yace ya Mulungu:

12 Cifundonso ndi canu, Ambuye:

Cifukwa Inu musudzula munthu ali yense monga mwa nchito yace.