Poopsedwa Davide athamangira Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Neginoto. Salmo la Davide.
1 Imvani mpfuu wanga, Mulungu;
Mverani pemphero langa.
2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga:
Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m’kutalika kwace.
3 Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pathawa mdani ine.
4 Ndidzagonera-gonerabe m’cihemamwanu;
Ndidzathawira mobisalamo m’mapiko anu.
5 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;
Munandipatsa colowa ca iwo akuopa dzina lanu.
6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu:
Zaka zace zidzafikira mibadwo mibadwo.
7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;
Mumpatse cifundo ndi coonadi zimsunge.
8 Potero ndidzayimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse,
Kuti ndicite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.