Madandaulo ndi pempho la Davide
Kwa Mkulu wa Nyimbo pa Susan-Eduti. Miktamu wa Davide; lakulangiza: muja analimbana nao Aramnabaraimu ndi Aramzoba, nabwera Yoabu napha a Edomu m’Ciagwa ca Mcere zikwikhumi mpilambu Ziwiri.
1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;
Mwakwiya; tibwezereni.
2 Mwagwedeza dziko, mwaling’amba:
Konzani ming’alu yace; pakuti ligwedezeka.
3 Mwaonetsa anthu anu zowawa:
Mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.
4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,
Aikweze cifukwa ca coonadi.
5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,
Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutibvomereze.
6 Mulungu walankhula m’ciyero cace; ndidzakondwerera:
Ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.
7 Gileadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;
Ndipo Efraimu ndi mphamvu ya mutu wanga;
Yuda ndiye wolamulira wanga,
8 Moabu ndiye mkhate wanga;
Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga:
Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine.
9 Adzandifikitsa ndani m’mudzi wa m’linga?
Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
10 Si ndinu, Mulungu, amene mwantaya?
Osaturuka nao makamu athu, Mulungu.
11 Tithandizeni kunsautso;
Kuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.
12 Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima,
Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.