Davide apempha cifundo kwa Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto, pa Seminiti. Salmo la Davide.
1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
Ndipo musandilange m’ukali wanu.
2 Mundicitire cifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine:
Mundicize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukuru;
Ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?
4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;
Ndipulumutseni cifukwa ca kukoma mtima kwanu.
5 Pakuti muimfa m’mosakumbukila Inu:
M’mandamo adzakuyamikani dani?
6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga;
Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;
Mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
7 Lapuwala diso langa cifukwa ca cisoni;
Lakalamba cifukwa ca onse akundisautsa.
8 Cokani kwa ine, nonsenu akucita zopanda pace;
Pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanaa,
9 Wamva Yehova kupemba kwanga;
Yehova adzalandira pemphero langa.
10 Adzacita manyazi, nadzanthunthumira kwakukuru adani anga onse;
Adzabwerera, nadzacita manyazi modzidzimuka,