Davide apempha Mulungu amlanditse, nadzinenera wosalakwa
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasbeti. Mikta mu wa Davide. Muja anatuma adikire nyumba yace, kuti amuphe,
1 Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga:
Ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.
2 Mundilanditse kwa ocita zopanda pace,
Ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.
3 Pakuti onani, alalira moyo wanga;
Amphamvu andipangira ciwembu:
Osacimwa, osalakwa ine, Yehova,
4 Osawapatsa cifukwa ine, athamanga nadzikonza;
Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.
5 Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli,
Ukani kukazonda amitundu onse:
Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.
6 Abwera madzulo, auwa ngati garu,
Nazungulira mudzi.
7 Onani abwetuka pakamwa pao;
M’milomo mwao muli lupanga,
Pakuti amati, Amva ndani?
8 Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;
Mudzalalatira amitundu onse.
9 Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;
Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.
10 Mulungu wa cifundo canga adzandikumika:
Adzandionetsa tsoka la adani anga.
11 Musawapheretu, angaiwale anthu anga:
Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,
Ambuye, ndinu cikopa cathu.
12 Pakamwa pao acimwa ndi mau onse a pa milomo yao,
Potero akodwe m’kudzitamandira kwao,
Ndiponso cifukwa ca kutemberera ndi bodza azilankhula.
13 Muwathe mumkwiyo, muwagurule psiti:
Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m’Yakobo,
Kufikira malekezero a dziko la pansi.
14 Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,
Nazungulire mudzi.
15 Ayendeyende ndi kufuna cakudya,
Nacezere osakhuta.
16 Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu;
Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa:
Pakuti Inu mwakhala msanje wanga,
Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
17 Ndidzayimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga:
Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa cifundo canga.