Davide adzudzula oipa Mulungu awalange
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasyeti; Miktamu wa Davide.
1 Kodi muli cete ndithu poyenera inu kunena zolungama?
Muweruza ana a anthu molunjika kodi?
2 Inde, mumtima mucita zosalungama;
Pa dziko lapansi mugawira anthu ciwawa ca m’manja mwanu.
3 Oipa acita cilendo cibadwire:
Asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.
4 Ululu wao ukunga wa njoka;
Akunga mphiri yogontha m’khutu, itseka m’khutu mwace.
5 Imene simvera liu la oitana,
Akucita matsenga mocenieratu,
6 Tyolani mano ao m’kamwa mwao, Mulungu:
Zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.
7 Apitetu ngati madzi oyenda;
Popiringidza mibvi yace ikhale yodukaduka.
8 Apite ngati nkhono yosungunuka;
Asaone dzuwa monga mtayo,
9 Miphika yanu isanagwire moto waminga,
Adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.
10 Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera cilango:
Adzasamba mapazi ace m’mwazi wa woipa.
11 Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama;
Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi.