Davide apempha Mulungu amciniirize, namlemekezapo
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasheti Miktamu wa Davide: muja anathawa Sauli au m’phanga.
1 Mundicitire cifundo, Mulungu, mundicitire cifundo;
Pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu:
Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu,
Kufikira zosakazazo zidzapita.
2 Ndidzapfuulira kwa Mulungu Wam’mwambamwamba;
Ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.
3 Adzanditumizira m’mwamba, nadzandipulumutsa
Ponditonza wofuna kundimeza;
Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.
4 Moyo wanga uli pakati pa mikango;
Ndigona pakati pa oyaka moto,
Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi,
Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.
5 Mukwezeke m’mwambamwa mba, Mulungu;
Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Anandichera ukonde apo ndiyenda;
Moyo wanga wawerama:
Anandikumbira mbuna patsogolo panga;
Anagwa m’kati mwace iwo okha.
7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;
Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.
8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze:
Ndidzauka ndekha mamawa.
9 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye:
Ndidzakuyimbirani mwa mitundu.
10 Pakuti cifundo canu ncacikuru kufikira m’mwamba,
Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
11 Kwezekani m’mwambamwamba, Mulungu;
Ulemerero wanu ukhale pamwamba m’dziko lonse lapansi.