Davide apempha Mulungu amlanditse; ayamika atamlanditsa
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yonat-Elem Recokimu, Miktamu wa Davide, muja Afilisti anamgwira m’Gati.
1 Mundicitire cifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza:
Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse:
Pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.
3 Tsiku lakuopa ine,
Ndidzakhulupirira Inu.
4 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:
Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;
Anthu adzandicitanji?
5 Tsiku lonse atenderuza mau anga:
Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.
6 Amemezana, alalira,
Achereza mapazi anga,
Popeza alindira moyo wanga.
7 Kodi adzapulumuka ndi zopanda pace?
Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8 Muwerenga kuthawathawa kwanga:
Sungani misozi yanga m’nsupa yanu;
Kodi siikhala m’buku mwanu?
9 Pamenepo adani anga adzabwerera m’mbuyo tsiku lakuitana ine:
Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.
10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:
Mwa Yehova ndidzalemekeza mau ace.
11 Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;
Munthu adzandicitanji?
12 Zowindira Inu Mulungu, ziri pa ine:
Ndidzakucitirani zoyamika.
13 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa:
Simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?
Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu
M’kuunika kwa amoyo.