Masalmo 55

Davide adandaula pa kuipa kwa adani, adziponya kwa Mulungu, nalangiza ena azitero iwo omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Zlrumbu. Cilanliizo ca Davide.

1 Cherani khutu pemphero langa, Mulungu;

Ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.

2 Mveram, ndipo mundiyankhe:

Ndiliralira m’kudandaula kwanga ndi kubuula;

3 Cifukwa ca mau a mdani,

Cifukwa ca kundipsinja woipa;

Pakuti andisenza zopanda pace,

Ndipo adana nane mumkwiyo.

4 Mtima wanga uwawa m’kati mwanga;

Ndipo zoopsa za imfa zandigwera.

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,

Ndipo zoopsetsa zandikuta.

6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa

Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.

7 Onani, ndikadathawira kutari,

Ndikadagona m’cipululu.

8 Ndikadafulumira ndipulumuke

Ku mphepo yolimba ndi namondwe.

9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:

Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m’mudzimo.

10 Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;

Ndipo m’kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.

11 M’kati mwace muli kusakaza:

Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m’makwalala ace.

12 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;

Pakadatero ndikadacilola:

Amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;

Pakadatero ndikadambisalira:

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,

Tsamwali wanga, wodziwana nane.

14 Tinapangirana upo wokoma,

Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.

15 Imfa iwagwere modzidzimutsa,

Atsikire kumanda ali amoyo:

Pakuti m’mokhala mwao muli zoipa pakati pao,

16 Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;

Ndipo Yehova atizandipulumutsa.

17 Madzulo, m’mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,

Ndipo adzamva mau anga.

18 Anaombola moyo wanga ku nkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere:

Pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,

Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe.

Popeza iwowa sasinthika konse,

Ndipo saopa Mulungu.

20 Anaturutsa manja ace awagwire iwo akuyanjana naye:

Anaipsa pangano lace.

21 Pakamwa pace mposalala ngati mafuta amkaka,

Koma mumtima mwace munali nkhondo:

Mau ace ngofewa ngati mafuta oyenga,

Koma anali malupanga osololasolola.

22 Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iyeadzakugwiriziza:

Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira ku dzenje la cionongeko:

Anthu okhetsa mwazi ndi acinyengo masiku ao sadzafikira nusu;

Koma ine ndidzakhulupirira Inu.